Sitikukana kuvomereza bajeti-Katsonga
by JOEL PHIRI - Saturday, July 21, 2007 - 12:39:02

PHUNGU wa nyumba ya malamulo woimira dera la kum’mwera m’boma la Neno, a Mark Katsonga Phiri, loweruka sabata latha adauza anthu a m’dera lake kuti aphungu wochokera mu zipani zotsutsa boma m’dziko muno sakukana kuvomereza ndondomeko ya momwe boma ligwiritsire ntchito ndalama kuyambira chaka chino mpaka chaka cha mawa.

Phunguyo adati aphunguwo akufuna kuti sipikala wa nyumba ya malamulo apereke kaye chigamulo pa nkhani yokhuza ndime 65 ya malamulo a dziko lino.

A Katsonga adalankhula izi pa msonkhano omwe adachititsa pa sukulu ya pulaimale ya Chipunga m’deralo.

Polankhula, iwo adati ndi bodza la nkunkhuniza lomwe anthu ena akufalitsa kuti zipani zotsutsa boma zagwirizana zofuna kugwetsa boma pokana kuvomereza ndondomeko ya za chuma choyendetsera dziko.

“Sikuti ife azipani zotsutsa boma tikukana kuvomereza ndondomekoyo koma chomwe ife tikupempha ndi chakuti sipikala achotse aphungu omwe adasintha zipani ndi kulowa zipani zina kuopa kuti ngati satero ndiye tibwerera ku ulamuliro wa chipani chimodzi” iwo adauza anthuwo.

Iwo adati cholinga chokhazikira ndime 65, yomwe imaletsa phungu wa nyumba ya malamulo kusintha zipani momwe angafunire, ndi kuteteza ulamuliro wa zipani zambiri m’dziko muno chifukwa akadapanda kutero aphungu onse otsutsa akadakalowa chipani cholamula cha Democratic Progressive Party (DPP) ndi cholinga chofuna mipando m’boma.

“Ngakhale ineyo ndimafuna nditakhala nduna yaboma koma kodi ngati nditasiya chipani changa cha Peoples Progresive Party (PPM) ndi kukalowa chipani cholamula cha DPP ndi ndani angamadzudzule boma litamachita zolakwira malamulo a dziko?” iwo adafunsa.

Iwo adauza anthuwo kuti ichi ndi chifukwa chake zipani zotsutsa boma zagwirizana kuti asadayambe kukambirana dongosolo la momwe boma ligwiritsire ntchito ndalama zake kuyambira mwezi uno ya Julaye mpaka chaka cha mawa, ayambe kaye akambirana nkhani yokhudza ndime 65 kuopa kuti akapanda kutero ulamuliro wa dziko lino ungathe kubwerera ku ulamuliro wa chipani chimodzi.

A Katsonga omwenso ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha PPM adati ngati sipikala angavomereze kuchotsa aphungu omwe adasiya zipani zawo ndi kukalowa zipani zina, aphungu otsutsa boma ndiwokonzeka kupita ku nyumba ya malamulo kukakambirana nkhani yokhudza dongosolo la za chuma.

“Koma chomwe ife otsutsa boma tisakuvomereza ndi chakuti aphungu omwe ali pa mulandu ophwanya malamulo a dziko lino akakambirane nawo nkhani yokhudza dongosolo la chuma komanso nkhani zina,” iwo adatero.

Nkhani yokhudza ndime 65 idagawanitsa nyumba ya malamulo masikuapitawo mpaka sipikala wa nyumbayo a Louis Chimango adangoganiza zotseka nyumbayo atawona kuti aphungu otsutsa boma amakakamira kuti sipikalayo achotse aphungu omwe adasiya zipani zawo omwe ambiri mwa iwo adalowa chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) chomwe mtsogoleri wake ndi pulezidenti wa dziko liko a Bingu wa Mutharika. Sipikala wa nyumba ya malamulo a Louis Chimango adalephera kuchotsa aphunguwo kaamba kakuti adakapempha khothi kuti Sipikala asawachotse kaye mnyumbayo.

<< back


 

Group Publications :


Website Redesigned and Hosted by