|
 |

‘Tidzipereka kulimbikitsa maphunziro a ana amasiye’
by
PRECIOUS MSOSA - Saturday, July 21, 2007 - 12:43:35
BUNGWE lothandiza ana amasiye la Carlos Cepeda Foundation lati lizipereka poyesetsa kutukula maphunziro a ana amasiye m’dziko muno pothandiza kupereka zipangizo zofunikira pa maphunziro awo.
M’modzi mwa akuluakulu a bungwelo lomwe liri ndi maziko ake m’dziko la America a Maureen Cepeda, ndi womwe adalankhula izi lachitatu sabata latha pa mwambo woperekera nyumba yodyeramo yomwe bungwe lawo lidamangira bungwe losamalira ana amasiye la YOSSA m’mudzi wa Mzumazi, mfumu yaikulu Mtema m’boma la Lilongwe.
Iwo adati ndi cholinga cha bungwe lawo kuwonetsetsa kuti ana amasiye nawonso akhale ndi mwayi opitiriza maphunziro awo ngati mwana aliyense, choncho ndi chifukwa iwo adadzipereka kutukula maphunziro a ana otero kudzera m’bungwe la YOSSA.
Iwo adati pozindikira kuti mwana aliyense ali ndi ufulu wa maphunziro, bungwe lawo lipitiriza kugwira ntchito zake m’dziko muno kudzera mu bungwe la YOSSA makamaka kumbali yotukula maphunziro a ana amasiye chifukwa nthawi zambiri sapitiriza maphunziro awo kaamba kosowa thandizo loyenera monga zipangizo zophunzirira.
Iwo adati ndi chifukwa bungwe lawo lidayamba ntchito yomapereka zipangizo monga yunifolomu komanso makope ndi zolembera kwa anawo ngati njira imodzi yowalimbikitsa pa maphunziro awo.
Bungwelo lidamanga nyumbayo ndi ndalama pafupifupi K500,000 komanso lidapereka zipangizo zophikira za mphamvu ya mpweya ndipo lakhala likupereka yunifolomu, makope, zolembera komanso sopo ndi zakudya kwa ana 250 omwe akusungidwa ndi bungwe la YOSSA. Bungwelo lidalonjeza kuti liyambanso ulimi wa nkhuku pa malopo ngati njira imodzi yoyesetsa kuthandiza malowo kuti azidzidalira paokha.
Poyankhulapo mkulu wa bungwe la YOSSA, a Fredrick Mkula, adati thandizo lomwe bungwe la Cepeda Foundation lakhala likupereka kuyambira chaka chatha lidathandiza ana ambiri kubwereranso ku sukulu.
Iwo adati m’deralo ana ambiri adasiya sukulu chifukwa chosowa thandizo ndipo adati adali wokondwa kuti pakadali pano chiwerengero cha ana amasiye opita kusukulu chidachuluka.
Iwo adawonjezeranso kupempha mabungwe ena m’dziko muno kuti adzitengapo mbali pothandiza ana amasiye pamaphunziro.
<< back
|
|
|
Group Publications :


|
Website Redesigned and Hosted by |
|
|