|
 |

Apempha mabungwe athandize asilikali odwala Edzi
by
JUSTICE MPONDA - Saturday, July 21, 2007 - 12:44:09
MKULU woyanga’anira za matenda a Edzi m’malo a asilikali a Cobbe Baracks m’boma la Zomba a Joseph Mdzinga adapempha mabungwe onse akufuna kwabwino kuti athandize malowo ndi chakudya chopatsa thanzi ndi cholinga chakuti atukulire umoyo wa asilikali omwe akulandira mankhwala a ARV ku malowo.
Mkuluyo adati thupi la munthu yemwe akudwala matenda a Edzi kuti ligwire ntchito bwino ndi kofunika kulandira zakudya zosiyanasiyana za magulu monga uchi, mkaka, mazira ndi zipatso zosiyanasiyana, zomwe akuti asilikaliwo mwaokha sangakwanitse kupeza.
A Mdzinga adalankhula izi loweruka sabata latha pa mwambo womwe amakambirana ndi bungwe la m’midzi losamalira anthu odwala matenda a Edzi la Sakata Green Care za momwe angapititsire pa tsogolo ntchito yosamalira anthu odwala matendawo.
Bungwe la achinyamata la Youth Net and Counselling (Yoneco) ndi lomwe lidakonza mwambowo omwe udachitikira m’mudzi mwa Chimwayi, mfumu yaikulu Mkagula m’bomalo.
A Mdzinga adati asilikali komanso anthu wamba okhala moyandikana ndi malowo oposa 572 ndi omwe akulandira thandizo la mankhwala a ARV pa chipatala cha ku maloko.
“Chomwe Amalawi onse angadziwe ndi chakuti msilikali aliyense odwala matenda a Edzi ndi wofunikirabe kwambiri ku chitetezo cha dziko lirilonse lomwe limakhulupilira mtendere ndi bata.
“Choncho boma lokha kudzera mu Malawi Defence Force silingakwanitse kuthandiza asilikali onse odwala matendawa, ndi chifukwa chake tikupempha anthu akufuna kwa bwino kuti atithandize,” iwo adatero.
Wapampando wa bungwe la Sakata Green Care, a Chrissy Mwanyali, adathokoza bungwe la Yoneco pokonza mwambowo chifukwa chakuti aphunzira zambiri za momwe angathandizire anthu odwala matenda a Edzi mwaokha kapena mosadalira bungwe lina liri lonse.
“Kudzera mu ndalama zomwe tidalandira kuchokera ku bungwe la National Aids Commission (Nac) komanso zipangizo za ulimi zomwe tidalandira kuchokera ku bungwe la Yoneco, tidakhazikitsa njira zopezera ndalama kukhala ndi minda ya chimanga, ya mpunga, komanso malo ophikira buledi.
“Pachifukwa chimenechi pakadali pano tikuthandiza anthu odwala matenda a Edzi okwana 204 ochokera ku midzi isanu yozungulira phiri la Sakata,” adatero a Mwanyali.
<< back
|
|
|
Group Publications :


|
Website Redesigned and Hosted by |
|
|