|
 |

Timu ya VTC Thunders iteteza chikho cha Old Mutual
by
MPHATSO MALIDADI - Saturday, July 21, 2007 - 12:44:50
TIMU ya VTC Thunders idateteza chikho cha masewero a volebo omwe imathandiza ndi kampani ya Old Mutual itangonjetsa timu ya VTC Veterans ndi zigoli zitatu kwa du pa masewero omwe adachitikira pa bwalo la Polytechnic Annexe mu mzinda wa Blantyre.
Aka kakhala kachitatu timu ya Thunders ikuteteza chikho chomwe adachikhazikitsa m’chaka cha 2005.
Kuti ifike mu ndime yomaliza, timu ya Thunders idangonjetsa timu ya Cobbe 3-0 pamene timu ya VTC Veterans idagonjetsa timu ya Naming’omba 3-1.
Timu ya Thunders idawonetsa kuti idali itakonzekera bwino chifukwa imasewera mwa pamwamba kuposa anzawo a Veterans.
Timu ya Thunders idalandira chikho ndi ndalama zokwana K40,000 pamene ya VTC Veterans idalandira ndalama zokwana K20,000 pokhala yachwiri.
Timu ya Naming’omba yomwe idagonjetsa timu ya Cobbe idalandira ndalama zokwana K20,000 pamene timu ya Cobbe idalandira ndalama zokwana K10,000.
Kaputeni wa timu ya Thunders a Crosberg Makondetsa adati iwo sadali wodabwa kuti adapambana.
A Makondetsa adati timu yawo ipitiliza kuteteza chikhocho paka kalekale.
Patsikulo adasakhanso anyamata amene adasewera bwino kuchokera ku matimu wosiyanasiyana ndipo adawapatsa mphotho zosiyasiyana.
Mwa ena wosewera bwino adali a Don Makonokaya, a Sinos Mpaso, a Albert Ngwira komanso a Maston Daza.
Mkulu wa bungwe lomwe limayendetsa masewerowo mu chigawo chakum’mwera a Pacharo Ngwira adati mpikisano wa Old Mutual ukuthandiza kutukula masewerowo m’dziko muno makamaka m’chigawocho.
Naye mkulu wa bungwe lomwe limayendetsa za masewero a volebo m’dziko muno a Jappie Mhango adapempha bungwe la chigawo chakum’mwera kuti liziyendetsa chikhocho potsatira ndondomeko zoyenera za ndalama.
Yemwe adayimilira kampani ya Old Mutual, a Naomi Kajamu, adalonjeza kuti kampani yawo iyetsetsa kuti ipitilize kuthandiza ligiyo.
<< back
|
|
|
Group Publications :


|
Website Redesigned and Hosted by |
|
|