|
 |

TIKAMBE ZA EDZI: Sabata lokumbukira za Edzi lithandiza kwenikweni
by
REX CHIKOKO - Saturday, July 21, 2007 - 12:46:25
NDIRI ndi chikhulupiliro kuti chaka chatha nkhani imeneyi ndidakambaponso powunikira ubwino woyezetsa magazi ndi kudziwa zotsatira ngati munthu ali ndi kachirombo ka HIV koyambitsa matenda a Edzi kapena ayi.
Mabungwe a boma komanso boma limakhala likuuza anthu kuti ndi bwino kuyezetsa magazi kuti munthu udziwe za tsogolo zomwe zingathandize kuti munthu adzitha kukonza ndondomeko zoyenera za moyo wake.
Ubwino wina woyezetsa magazi ndi wakuti munthu umakhala ndi udindo woonetsetsa kuti kachirombo ka HIV kasapitilire kufalikira chifukwa chakuti kwa munthu amene akudziwa kuti ali ndi kachirombo ka HIV ndi bwino kuti azidziteteza komanso kuteteza ena pa nthawi imene akugonana.
Nkhani yaikulu ndi yakuti kumafunika kudziteteza ndi kuteteza munthu wina mwakutero ndiye kuti kachirombo ka HIV sikangapitilire kufala.
Chaka chino, monga zidaliri chaka chatha, palibe chomwe boma likupereka kwa anthu, kapena tinene kuti chilimbikitso china chiri chonse kuti akayezetsa magazi boma lithandiza munthuyo mwa njira iti.
Kuyezetsa magazi si ntchito yaikulu. Imatha mphindi zochepa basi, limeneri sivuto koma vuto liri pa zotsatira zake zoyezetsa magazi.
Sindikudziwa kuti boma chaka chino lakhazikitsapo mfundo zotani kwa anthu amene atawapeze kuti ali ndi kachirombo ka HIV. Ndikudziwa kuti sionse amene pakadali pano ali ndi kachirombo ka HIV amene akufunika thandizo la mankhwala koma ndi bwino kuti boma likhazikitse ndondomeko yabwino yakuti munthu akamupeza kuti ali ndi kachirombo adzitha kulandira thandizo mwansanga.
Aliyense akudziwa kuti anthu ambiri amwalira osati chifukwa cha matenda a Edzi kapena matenda aliwonse amene amadza chifukwa cha mliriwo koma kuti anthu akufa chifukwa cha nkhawa, kusowa chikondi, kusowa chilimbikitso komanso tsogolo choncho ndi bwino kuti boma linganizire njira imeneyo koposa kumangowayeza anthu ndi kuwasiya kuti azifa ndi nkhawa.
<< back
|
|
|
Group Publications :


|
Website Redesigned and Hosted by |
|
|