CHIKOKO PA CHIKOPA: Bullets izipereka zifukwa zokwanira
by REX CHIKOKO - Saturday, July 21, 2007 - 12:47:10

NTHAWI ina iliyonse, chaka chino, timu ya Bullets imati ikagonja mphunzitsi wa timuyi komanso anyamata osewera mu timuyi akumapereka nkhani kuti timu yawo sikuchita bwino chifukwa cha vuto la za chuma.

Chaka chino chokha timu ya Bullets yagonja masewero atatu. Awiriwo ndi matimu ang’onoang’ono kwambiri yachitatu ndi timu ya Red Lions.

Ngati munthu amene ndimadziwa zomwe zimachitika kwa munthu akakumana ndi mavuto a za chuma ndimaganizo kuti zomwe akunena aku Bullets ndi zoona.

Mavuto a za chuma amazunzitsa munthu, mavuto a za chuma amachotsa munthu ulemu kotero kuti ndi ana omwe amatha kumamunyoza munthuyo.

Zonsezi ndi zomwe zakhala zikuchitikira timu ya Bullets.

Koma ndasiya kukhulupilira zomwe timuyi ikumauza anthu kuti ikumagonja chifukwa cha mavuto a za chuma.

Ndi bwino kuti aku Bullets avomereze kuti nthawi zina timu yawo ikumakumana ndi mikwingwirima malinga ndi ukatswiri wa anzawo m'bwalo la za masewero osati ku mbali ya chuma.

Chomwe chandichititsa kuti ndiyambe kukayikira zomwe imalankhula timu ya Bullets ndi kupambana kwawo pa masewero a pakati pa timuyo ndi adani awo aakulu, MTL Wanderers, komanso kugonja kwa timuyo kwa asilikali ku Zomba.

Ngati Bullets yomwe akuti idalibe ndalama, idapambana bwanji ndi Wanderers komaso zidatheka bwanji kukagonja ku timu ya Red Lions ndalama ziri m'nthumba.

Chomwe ndikufuna kunena apa ndi chakuti timu ya Bullets isamanamizire umphawi wake ikagonja uku ndi kuchepetsa matimu ena amene achita bwino pomagwiritsa ntchito mau a chisoni kuti anthu asawone kulephera kwa timuyo.

Mwachidule timuyo idagonja ku matimu a Eagle Strikers komanso Red Lions chifukwa chakuti anyamata wosewera matimu awiriwo adasewera bwino osati chifukwa chakuti Bullets idalibe, kaya ilibe ndalama.

Timu ya Bullets izitha kuvomereza kugonja ndi kuyamikira anzawo akasewera bwino osamabweretsa umphawi wakunyumba mu masewero a mpira.

<< back


 

Group Publications :


Website Redesigned and Hosted by