Bullets ikumananso ndi Manoma mawa
by PETER KANJERE - Saturday, July 21, 2007 - 12:48:03

MAWA kulinso masewero a nkhodzo za pusi pamene matimu a MTL Wanderers ndi Big Bullets akukumananso pa bwalo la za masewero la Kamuzu mu mzinda wa Blantyre.

Masewerowo akhala amu ndime ya kota fainolo ya chikho cha bungwe la Fam chomwe amathandiza ndi a banki ya Standard.

Aka kakhala kachiwiri pa masiku asanu ndi atatu kuti matimu awiriwo akumane.

Matimu awiriwo adakumananso loweruka sabata latha pamene timu ya Bullets idakutumula timu ya MTL Wanderers ndi zigoli zitatu kwa chimodzi pa mpira wa TNM Supa Ligi omwe udakokera chikhamu ku bwalo la masewero la Kamuzu.

Wochemerera a timu ya Bullets adaimba ndi kuvina pokondwerera kupambanako komwe ndi koyamba kugonjetsa Bullets mu Ligi patadutsa zaka ziwiri.

Timu ya Bullets ndiyo idayamba kumwetsa chigoli pamene m’nyamata wosewera kutsogolo Charles Ngosi, yemwe chaka chatha adali mu timu ya Wanderers, adaswa bomba atalandira mpira kuchokera kwa mnzake Grant Lungu m’chigawo choyamba.

Posafuna kugonja, Wanderers kapena kuti Manona, adabweza kudzera mwa Victor Nyirenda atalandira mpira kwa Joel Chipofya chakumanja.

Chigawo choyamba chidatha.

Bullets idabwera ndi mkwiyo m’chigawo chachiwiri pamene Ngosi adasonyeza kuti ndi ngozi pamene adagoletsa ndi mutu atalandira mpira kuchokera kwa Majeed Sanudi.

Chigoli chachiwiricho chidaso-konezeratu mutu timu ya Wanderers ndipo zithu zidavuta kwambiri pamene Lungu adabwiza wotseka kumbuyo wa Wanderers Chembe Zidana kenako ndi kudyetsanso kalulu golokipala Valence Kamzere ndi kuchinya chigoli chachitatu.

Chisangalalo cha Bullets sichidakhalitse pakuti mawa lake idagonja ku timu ya asilikali ya Red Lions ku Zomba.

M’nyamata Dan Ziba ndiye adachita chipongwe timu ya Bullets pogoletsa chigoli chimodzi cha asilikaliwo.

Zinthu zidayendako bwino kwa timu ya Wanderes pakuti idapambana pamasewero ake ndi Blue Eagles ndi zigoli ziwiri kwa chimodzi.

Moses Chavula ndi Victor Nyirenda ndi omwe adagoletsa zigoli za Wanderers pomwe Musakaike Mlenga ndiye adapukuta misozi ya Blue Eagles.

M’masewero ena timu ya Silver Strikers idalepherana ndi timu ya Civo United pamene timu ya Escom United idapambana ndi chigoli chimodzi pamasewero ake ndi timu ya Dwangwa United.

Pakadali pano timu ya Wanderers ikutsogola ndi mapointi 21 motsatiridwa ndi timu ya Silver ndi mapointi 18 mofanana ndi timu ya Escom pamene Bullets ili ndi mapointsi 17.

<< back


 

Group Publications :


Website Redesigned and Hosted by